Woyang’anira ndende ku Nsanje, Albert Blackson, ali m’manja mwa apolisi chifukwa chomuganizira kuti waba kanema wawayilesi woperekedwa kwa akaidi kundende ya Nsanje.
Mneneri wa polisi ku Nsanje, Agnes Zalakoma, watsimikiza za kumangidwako; ponena kuti woganiziridwayo ayankha mlandu wakuba.
Malinga ndi malipoti, ali pa ntchito,. woganiziridwayo adatulutsa skrini ndikupereka kwa chibwenzi chake mkati mwa boma la Nsanje; kumunamiza kuti mkazi wake wasesa zonse mnyumba mwake kusiya screen basi.
Zanenedwanso kuti mtsikanayo adakauza Blackson kupolisi atazindikira kuti ali kunja kukasaka makasitomala oti agule skriniyo ndipo adatenga nthawi yayitali kuti abwerere.
Blackson comes from Bereu village in the area of Traditional Authority Maseya in Chikwawa.