Apolisi agwila anthu osongola kapena kuti athayiming’i m’malo akulu okwelera bus amumzinda wa Lilongwe lachisanu sabata yatha, apolisi mumzindawu lero agwilanso anthu ena 16 ochita m’chitidwe monga omwewu
Mneneri wapolisi ya Lilongwe, Inspector Hastings Chigalu wati mwa anthuwa 12 ndi amuna pamene anayi ndi akazi.
Chigalu wati ntchito yogwila anthuwa lero inatsogoleredwa ndi mkulu wapolisi ya Lilongwe a Clement Gulo.
Iye wati anthuwa akuyembekezela kukaonekela kubwalo lamilandu sabata yam’mawa ndipo akayankha mulandu ochita zinthu zofuna kubweretsa chisokonezo pamalo, zomwe ndizosemphana ndi gawo 181 lamalamulo adziko lino.
Sabata yatha apolisi mumzindawu anagwila anthu ena 20 omwe amasongola kapena kuti kupanga thayiming’i muma bus omwe amayima mudepoti yaikulu ya Lilongwe.