Bungwe la Center for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) ndi amalonda ang’onoang’ono ku Blantyre aimitsa ziwonetsero zomwe zidakonzekera lero mumzinda wamalondau.
Malinga ndi mkulu wa bungwe la CDEDI, a Sylvester Namiwa, wati kuyimisaku kwabwela chifukwa potsatira nkhani yazovuta zomwe zatigwela maka maka ndizomwe analankhula Purezidenti Lazarus Chakwera pomwe adalamula masiku atatu olira maliro a nduna a Sidik Mia ndi a Lingson Belekanyama.
Namiwa powauza atolankhani adati ziwonetserozi zichitika Lachiwiri sabata yamawa pa 19 Januware 2021 ponena kuti akufuna kuti madandaulo awo alankhulidwe ndi boma lotsogozedwa ndi Chakwera.
“Center for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) mogwirizana ndi Blantyre Small Scale Business Operators, potero akudziwitsa dziko lino kuti ziwonetsero zamtendere zomwe zimyenela kuchitika Lachitatu, 13 Januware, 2021, zaimitsidwa Lachitatu, 20 Januware 2021.
Boma la Tonse alliance likudutsa munyengo zovuta zomwe zikuonesa ngati mabungwe oyan’anila zaufulu sakukondwa nazo