Akubanja la Bagus omwe ali Makolo ake a Malemu Waheeed Bagus ati akufuna Chilungamo chiwoneke pa imfa ya mwana wawo.
William Phiri adapha Chibwezi chake Waheed Bagus pomuwombera ndi Mfuti pa Mimba.
Mongokumbutsa – William Phiri adali pa Ubwezi ndi Mtsikana okongola mukumuonayi Waheed ndipo anthuwa adagwirizana kuti akwatilane.
William adagulira Chibwezi chakechi Galimoto ya Mtundu wa Benz C180 ndipo idali yapamwamba kwambiri.
Koma chomwe chidatsitsa dzaye kuti mamunayi afike pomupha mkaziyu ndi choti.Padali pa 15 December ku Lilongwe Mkaziyu adamuuza Chibwezi chakechi william kuti akukashopa zinthu mu Tawoni ya Lilongwe ndipo uwu udali ulendo wa ku Lodge ndi Mamuna winanso wa Chibwezi ndipo adapita ku Lodge uko ndi Galimoto yomwe William adamugulira ija.
Anthu ena awugogodi adamuyimbila William Foni kuti athamange adzagwire Chigololo Mkazi wake ndipo William atafika ku Lodge iyo adamupeza mkaziyu ali ndi Mamuna wa Chibwezi nthawi yomwe William adamuwombera Mkaziyu pa Mimba ndipo arakhala mu Chipatala kwa Mwezi umodzi ndi pamene amamwalira.
Koma nkhani yomwe pano ikuvuta ndi yoti Willam adatulutsidwa pa Bail kalekale ndipo nkhaniyi ikuoneka ikumwa Madzi ndipo zapangitsa achibale omwe ali Makolo a Waheed kukamang’alanso ku bwalo la Milandu kuti agwire ndikutsekera William kuti alandile Chilango.