Mtsogoleri wa Chipani chotsutsa boma, Kondwani Nankhumwa yemwenso ndi Wachiwiri kwa Purezidenti wa Democratic Progressive (DPP) waku Mwera afotokoza zakukhumudwa ndi imfa ya anthu 21 pangozi yapamsewu ku Lizulu ku Ntcheu.
Polemba patsamba lake la facebook a Nankhumwa adati: “Ndikudandaula komanso kusakhulupirira kuti ndalandira uthenga wachisoni wawalira wa anthu pafupifupi 21 pangozi yowopsa yamagalimoto yomwe idachitika m’mawa wa Lamlungu, Ogasiti 1, 2021 pafupi ndi Lizulu ku Ntcheu.
“Ndikufuna kutumiza mawu anga achisoni kuchokera ku mabanja onse omwe aferedwa.
“Ndikumva chisoni kwambiri kumva kuti ambiri mwa anthu omwe amwalira anali ochokera kubanja limodzi. Mzimu wawo wabwino upumule mwamtendere.
“Kwa iwo omwe avulala mosiyanasiyana, pemphero langa kwa Mulungu Wachikondi Kwambiri ndikuti muchiritse msanga. Ndikuyembekezera mwachidwi kuti muchire ndikupitilizabe kuthandiza pantchito zachitukuko komanso zachuma mdziko lathu lokongolali. ”
Pakadali pano Mtsogoleri wa Dziko lino Dr. Lazarus Chakwera alengeza za kulira kwa maliro a masiku awiri.